Gwamba walapaso
This article was originally published on Malawi24 ">Malawi24, Malawi's #1 independent news platform. “Moti nthawi yoseyi mumatsitsimula miyoyo kwinaku mukukonkha?” Achuluka mafuso pa zomwe woyimba nyimbo zauzimu koma zogwira palisani, Duncan Zgambo, wotchedwaso kuti Gwamba wanena. Woyimba Gwamba waulura kuti wakhala akukokera anthu ku ufumu wa Mulungu kwinaku akukonkha chakumwa chaukali. Izi ndi malingana ndi zomwe “Landlord” walemba patsamba lake la fesibuku. Lolemba madzulo, Zgambo yemweso ama
AI summary
“Moti nthawi yoseyi mumatsitsimula miyoyo kwinaku mukukonkha?” Achuluka mafuso pa zomwe woyimba nyimbo zauzimu koma zogwira palisani, Duncan Zgambo, wotchedwaso kuti Gwamba wanena.
Woyimba Gwamba waulura kuti wakhala akukokera anthu ku ufumu wa Mulungu kwinaku akukonkha chakumwa chaukali.
Izi ndi malingana ndi zomwe “Landlord” walemba patsamba lake la fesibuku. Lolemba madzulo, Zgambo yemweso amadzitchaso kuti G.O.A.T adadzidzimutsa gulu pomwe adalengeza kuti wasiya kumwa bibida.
“I WILL NEVER DRINK ALCOHOL AGAIN. (Sindidzamwaso mowa),” watelo Gwamba polapa.
Paja mbuto ya kalululu idakula ndi tadzaonani, m’kuthwanima kwa diso anthu adaitanizana ndipo ndemanga zidafumbula pa tsambali.
Ambiri mwa anthu omwe ayikira ndemanga pa tsambali awonetsa kudabwa ndi zomwe woyimbayu walembazi.
“So you’ve been gospeling while drinking holy water😅 (Moti wakhala ukuimba zauzimu ndikumamwaso mowa?),” uno kunali kudabwatu kwa Kelvin Mnkhumbwe, m’modzi mwa oyikira ndemanga.
Naye Happy Kamanga wati wakhala akuganiza kuti Gwamba adasiya kumwa mowa kuyambira pomwe adalengeza kuti wabadwa mwatsopano, wayamba kuimba nyimbo zauzimu. “Thought you stopped a long time ago? 😅😅”
Ena mwa anthu omwe ayikira ndemanga ati woyimbayu akungoserewula chabe ponena kuti munthu wofuna kusiya kumwa mowa samachita kulengeza.
Izi zikubwera pomwe mu 2021, Gwamba adalengezaso kuti wasiya kumwa mowa komaso mankhwala ozunguza ubongo.
Follow the story
About this article
- Length
- 193 words · 1 min read
- Published
- September 8, 2026
- Byline
- Malawi24 Reporter
- Source
- Malawi24