Lamya za m’manja za omwe adali m’ndege ya asilikali a nkhondo yomwe idagwera ku Chikangawa zikadapezeka msanga n’kuchitidwa chipikisheni zidakatha kuthandiza kupeza chilungamo cha ngoziyo.
Umu ndimo katswiri wodziwa zamafoni ndi chipikisheni pogwiritsa ntchito makina a makono a Kingsley Goliati adafotokozera komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo yomwe ikufufuza za ngoziyo Lachiwiri.
Nyumba ya Malamulo yapatsidwa udindo wofufuza mayankho okhudza ngozi yoopsa ya ndege. | Nation
“Zinthu ngati lamya za m’manja zimasunga umboni wofunikira kwambiri moti kuzipeza msanga n’kufufuzamo, zikhoza kuthandiza kupeza mayankho a chomwe chidachitika ndege isadagwe,” adatero a Goliati.
Umboniwo ukubwera abale ndi okondedwa a ena mwa omwe adafa pa ngoziyo atauza kale komitiyo kuti padali matatalazi kuti apatsidwe lamya za abale awo komanso lamya zina zidawongongekeratu.
Koma a Goliati adati kuphwanyika kwa lamya ndi kusokonekera kwa uthenga wina mu lamyazo sikungasokoneze kafukufuku wogwiritsa ntchito makina a makono.
“Chofunika ndi mgwirizano pakati pa nthambi zosiyanasiyana monga nthambi yazatekinoloje ku polisi, nthambi za boma za Macra komanso MRA malingana ndi kafukufuku wake,” adatero a Goliati.
Yemwe adali wachiwiri kwa pulezidenti m’boma lapitalo a Saulos Chilima ndi anthu ena 8 adafera pa ngoziyo, yomwe idachitika pa 10 June 2024 m’nkhalango ya Chikangawa.
Mayi Mary Chilima, mkazi wa a Chilima, adauza komitiyo kuti padatha mwezi watunthu asadaone lamya za amuna awo komanso zidabwera zili zowonongeka.
Iwo adauza komitiyo kuti kuchedwa kuwapatsa lamyazo kumawapatsa maganizo kuti mwina nthawi yomwe zidali m’manja mwa boma, umboni wina udasowetsedwamo.
“Ndidayamba kulondoloza kuti bwanji lamyazo sizimabwera ndipo patatha mwezi adatipatsa lamya ziwiri zokha pomwe imodzi sitikudziwa kuti ili kuti,” adatero a Chilima.
Mayi Sarah Lapukeni, omwe adali mkazi wa yemwe adali wachiwiri kwa wa za ndondomeko ku unduna wa ubale wa Malawi ndi maiko ena a Abdul Lapukeni omwe adali nawo mu ndegeyo, adati lamya ya amuna awo idabwezedwa ili sanza zokhazokha.
“Kuyiona lamyayo ngati amachita kusinja mu mtondo. Zidali zodabwitsa kuti kupindika kumeneko ndi ngozi yomweyo?” adatero mayi Lapukeni.
Mayi Effiness Katunga Kanyemba, mkazi wa malemu Dan Kanyemba omwenso adali mundegeyo chifukwa adali dotolo wa a Chilima, adati lamya ya amuna awo idabwera ili sanza.
Iwo adauza komitiyo kuti tsiku la ngoziyo adaimba lamya ya amuna awo m’ma 4 koloko madzulo ndipo idaitana mpaka kuduka ndipo podzaimba kachiwiri idali yothima.
Yemwe adali mlembi mu ofesi ya wachiwiri kwa apulezidenti a Luckie Sikwese adauza komitiyo kuti adatumizira a Chilima uthenga pa lamya nthawi ya 11.37 mmawa koma siyidayankhidwe.
The post ‘Lamya zikadathandiza kafukufuku wa ndege’ appeared first on Nation Online.
Follow the story