
This article was originally published on Malawi24 ">Malawi24, Malawi's #1 independent news platform. “Mtengwa wasanduka mwiniwake wa munthu ndipo watenga ulamuliro wambirii wa Manda a m’bale wathu Lucius Banda.” Uku nkulira kwa nzirazembe pa maimbidwe Paul Banda pomwe nkhani ya chiriza cha malemu Lucius Banda yamanga nthenje. Mu kilipi yomwe yafala mmasamba amchezo, Paul wati a kuchikazi kwa malemu Lucius akhala akuchita zinthu zina zomwe zakhala zikumudetsa kukhosi. […] Read the full article an
“Mtengwa wasanduka mwiniwake wa munthu ndipo watenga ulamuliro wambirii wa Manda a m’bale wathu Lucius Banda.” Uku nkulira kwa nzirazembe pa maimbidwe Paul Banda pomwe nkhani ya chiriza cha malemu Lucius Banda yamanga nthenje.
Mu kilipi yomwe yafala mmasamba amchezo, Paul wati a kuchikazi kwa malemu Lucius akhala akuchita zinthu zina zomwe zakhala zikumudetsa kukhosi.
Mwazina, iye wati Lucius atamwalira mu 2024, akuchikaziwa ankafuna malemuwa ayikidwe pakhomo, zomwe iye pamodzi ndi anthu ena akuchimuna adakanitsitsa mwantu wagalu.
“Ine ndidawauza kuti Lucius akuyenera kukagona komwe makolo akeadagona. Iye uja anali ngati mfumu ndiye ayenera kukagona pakati pa anthu ake,” watelo Paul.
Mkulankhula kwake Paul wati Lucius akadakhala kuti ankufuna kuti akadzamwalira adzayikidwe pakhomo akadatha kumufotokozera.
“Ine ndi Lucius timakambirana chirichonse kotero kunali kosavuta kundiuza za ganizo loti adzaikidwe pakhomo akadzamwalira, koma sadandiuzepo maganizo ili,” watelo Paul.
Iye wati ganizo la akuchikazili litakanika, panakhala kukanukana pakati pa mbali ziwirizi, ndipo wati pomwe iye wakhala akudwala palibe wakuchikazi yemwe adakamudwazikapo kapena kungomuzondapo mchipatala.
“Ndimalumidwa ndi udzudzu (ndili ku Lilongwe) nyumba ya Lucius ilipo ku 10 kuja,” wadandaula Paul.
Iye wati zambiri zokhudza mwambo okumbukira Lucius kapena nkhani yokhudza chiriza wakhala akuzimvera m’masamba a mchezo, zomwe wati zakhala akudabwa pomwe wati aliyense wa kumtundu wawo samawuzidwako.
“Chiyembekezero chathu chinali choti atiyitana ngati akuchimuna kuti tikambirane zosonkha, koma zonsezi panalibe ndipo zimaoneka kuti akuzikonza okha akuchikaziwo kuti ife zisatikhudze ayi, ndipo timangomva ma date.
“Komwe kudachokera ndalama zomangira Chiliza situkudziwa, a kuchikazi adatseka ndi kutchinga paliponse kuti akuchimuna asatenge nawo gawo lirilonse, ndipo amachita chilichonse mmene akufunira” watelo Paul.
Tate pa mayimbidweyu wati sikoyenera kunyoza mfumu Sosola ya ku Balaka ponena kuti zomwe yachita zomanga mpanda wa mitengo pa chiriza cha Lucius sizolakwika.
Paul wati iye akuona kuti akuchikazi adali ndi zolinga zofuna kugwiritsa ntchito manda a Lucius ngati dimba lopezerapo ndalama zothandizira Lucius Banda Foundation.
Follow the story